Mneneri wa nthambiyi, a Yobu Kachiwanda, wanena izi potsatira uthenga omwe akuluakulu azanyengo ku Zimbabwe apereka kwa mzika za dzikolo kuti kukhala ng’amba kuyambira Lachisanu sabata yatha mpaka pa 2 Febuluwale.
A Kachiwanda ati ngakhale maiko a Malawi ndi Zimbabwe amakhala ndi nyengo yofanana, dziko lino lipitilira kulandira mvula ya mlingo wochuluka monga momwe analengezera m’mwezi wa September chaka chatha.