Print this page

Mvula Ipitilira

Nthambi yoona zanyengo m'dziko muno yati palibe nkhawa iliyonse ya ng’amba mwezi uno wa January. 

Mneneri wa nthambiyi, a Yobu Kachiwanda, wanena izi potsatira uthenga omwe akuluakulu azanyengo ku Zimbabwe apereka kwa mzika za dzikolo kuti kukhala ng’amba kuyambira Lachisanu sabata yatha mpaka pa 2 Febuluwale.

A Kachiwanda ati ngakhale maiko a Malawi ndi Zimbabwe amakhala ndi nyengo yofanana, dziko lino lipitilira kulandira mvula ya mlingo wochuluka monga momwe analengezera m’mwezi wa September chaka chatha.

Read 1631 times
Login to post comments