Print this page

Loya Wati Athandiza Mayi waku Mchinji Yemwe Apolisi Anamumanga Pamodzi ndi Khanda Lake

Loya wina Alexious Kamangila ,wadzipereka kuti ayimira mwaulere mayi wa zaka 30 ku Mchinji, yemwe wakhala akusungidwa ndi a polisi pamodzi ndi mwana wake pa mlandu wonyanyalira mwamuna khanda.

A Kamangila, omwe ndi mphunzitsi ku univesite ya Malawi, ati atawerenga nkhani ya maiyu pa Zodiak Online aganiza zomuimilira kuti athandizire chilungamo pa nkhaniyi.

A Matilda Chirwa, omwe pano ali pa belo, dzulo anakawonekera ku khothi komwe wachiwiri kwa Magistrate Anne Simwaka wayimitsa mlandu-wu mpaka lachisanu sabata ya mawa pofuna kulola oyimira boma pa mlanduwu kuti abweretse mboni.

Pakadali pano, magistrate Simwaka wagwirizana ndi pempho la loya-yu kuti mayiyu akamuwunike achipatala, ngati kumangidwa kwake sikunasokoneze kaganizidwe kake komanso umoyo wake poti anali atachira chakumene.

Read 2297 times

Last modified on Thursday, 10/08/2023

Login to post comments