NBS Yawonjezera Makobili a Chikho
Bank ya NBS lero yalengeza kuti yakweza ndalama zomwe imapereka pa mpikisano wa mpira wa miyendo wa ntchito zachifundo (Charity Shield) kuchoka pa K20 million kufika pa K40 million m’zaka zitatu zikudzazi.
Mkulu wa bankiyi a Kwanele Mgwenya walengeza izi kwa atolankhani azamasewero mu mzinda wa Blantyre, komwe anati kukweraku ndi kaamba koti bungwe loyendetsa masewero a mpira wamiyendo la FAM likugwira bwino ntchito yake m’dziko muno.
Mlembi wa bungwe la FAM a Alfred Gift Gunda wati ndiokondwa ndi izi.
Ndalamazi pakutha pa mpikisanowu chaka chino azigwilitsa ntchito yotukula maphunziro a asungwana.
Timu za FCB Nyasa Bullets ndi Silver Strikers ndi zomwe zisewere masewerowa chaka chino.
Last modified on Wednesday, 13/03/2024