A Nankhumwa, Jeffrey ndi Ena Awachotsa mu DPP
Chipani cha DPP chachotsa m'chipanichi ena mwa akuluakulu ake monga a Kondwani Nankhumwa, a Grezelder Jeffrey, a Mark Botomani, a Nicholas Dausi ndi a Ken Msonda mwa ena.
Malingana ndi kalata yomwe chipanichi chatulutsa Loweruka, izi zadza pumbuyo pa zokambirana zomwe akulu akulu a komiti yosungitsa mwambo m’chipanichi analinazo masiku apitawo ndi adindowa.
Onse omwe awachotsa mu DPP ndi khumi ndi m’modzi.
Koma a Ken Msonda, mmodzi mwa omwe awachotsa, ati zachitikazi ndi zolakwika, ndipo ati mwina kunali bwino anthuwa anakangowayimitsa m’maudindo awo.