Mboni za Yehova Zatulutsa Baibulo la M’ciyao

Kwa anthu ambiri amene anasonkhana pa malo ochitira msonkhano a Mboni Za Yehova ku Lilongwe ndi ena amene analumikizidwa m’mipingo yosiyanasiyana m’Malawi komanso mayiko oyandikira, June 14, 2026 ndi tsiku limene adzalikumbukira mwapadera popeza analandira mphatso ya Baibulo la Dziko Latsopano m’Chiyao.   

Kunali chisangalalo komanso kuomba mmanja kochokera pansi pa mtima pamene kutulutsidwa kwa Baibuloli m’Chiyao komanso Buku la Uthenga wabwino la Mateyu mu chilankhulo cha Lambya  ndi Kyangonde kunalengezedwa. 

Kwa ambiri amene anamvetsera msonkhanowu, uku sikunali kutulutsidwa kwa Baibulo chabe koma umboni wakuti Yehova amawakonda ndi kukwaniritsa loto lawo lofuna kulalikira komanso kuphunzira mau a Mulungu m’chilankhulo chimene amachimva bwino kwambiri. 

Msonkhanowu unafika pachimake pamene Gage Fleegle wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni Za Yehova analengeza za kutulutsidwa kwa Baibuloli, lomwe likuyembekezeka kuthandiza anthu ambiri amene amalankhula Ciyao ku Malawi, Mozambique ndi Tanzania.  

Baibuloli likupezeka m’njira zingapo: lochita kusindikiza, lowerenga pa intaneti kapena kompyuta ndi lamya za m’manja komanso lomvetsera.

Msonkhanowu unaliso osangalatsa kwa anthu pafupifupi 100 000 amene amalakhula chi Lambya ndi 150 000 amene amalankhula Kyangonde popeza nawonso alandira Buku la Uthenga wabwino la Mateyu lomasulilidwa m’zilankhulo ziwirizi, malinga ndi a Given Chichitike, mneneli wa Mboni Za Yehova mchigawo cha pakati cha dziko lino.

“Kutulutsidwa kwa Baibuloli kutithandiza kwambiri pa ntchito yathu yolalikira chifukwa anthu amakhudziwa kwambiri akamva Mau a Mulungu m’chilankhulo chawo choncho tikukhulupilira kuti mphatso imene Yehova waperekayi ichititsa kuti anthu ambiri a zilankhulozi awamvetse bwino Mau a Mulungu n’kumatsatira zimene amanena,” atero a Chichitike. 

Kutulutsidwa kwa Baibuloli ndi mbali imodzi ya ntchito imene a Mboni Za Yehova akuchita padziko lonse poonetsetsa kuti Baiblulo la Dziko Latsopano limene likupezeka lonse Kapena m’chigawo chabe m’zilankhulo zoponsa 339, lamasulilidwa m’zilankhulo zambiri n’kuthandiza anthu kumva Mau a Mulungu.

Online Journalist's Avatar

Online Journalist

ZODIAK ONLINE

ArtBridge House, Area 47
Sect. 5, P/Bag 312
Lilongwe, Malawi
Text: (265) 999-566-711
support@zodiakmalawi.com

Information

Quick Links

Follow Us

Login

{loadmoduleid ? string:? string:? string:16 ? ? ?}